Atsogoleri azipembedzo zosiyanasiyana alimbikitsa umodzi pakati pa aMalawi, pomwe patha chaka chimodzi dziko lino litakumana ndi namondwe wa Freddy.
Ena mwa alalikiwa ndi Phophet Shepherd Bushiri, M’busa Biswick Nkhoma yemwe ndi Moderator wa CCAP General Assembly, Sheikh Swalley Chilundu a Muslim Association of Malawi ndi ena.
Iwo athokoza Prezidenti Dr Lazarus Chakwera kamba kopempha thandizo kwa anthu ndi mabungwe kuthandiza dziko lino pa nthawi ya Namondwe.
Iwo apemphanso aMalawi kuti asataye mtima mu nyengo zonse zimene dziko lino lakhala likukumana nazo.
Olemba: Blessings Cheleuka