Apolisi m’boma la Mangochi amanga a Rashid Mailosi a zaka 18 ndi a Paul Edward a zaka 19 powaganizira kuti anathyola nyumba yogulitsira katundu ndi kubamo katundu wandalama pafupifupi K500,000.
Ofalitsa nkhani pa polisi ya Mangochi, Amina Tepani Daudi, watsimikiza nkhaniyi ndipo wati awiriwa akaonekera kubwalo lamilandu kukayankha mulandu wakuba.