Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Anthu 87 a zipani zosiyanasiyana alowa MCP ku Mangochi

Anthu osachepera 80 ochokera zipani za DPP, UDF ndi zina alowa chipani cholamula cha Malawi Congres (MCP) ku Mangochi.

Powalandira anthuwa, yemwe ali wachiwiri kwa mkulu wa chipanichi ku chigawo cha kummawa, a Hassan Chikuta, anati anthu akulowa chipani cha MCP chifukwa cha mfundo zake zokhwima komanso anthuwo aona zitukuko zosiyanasiyana zomwe boma la President Lazarus Chakwera lachita ku Mangochiko.

A Chikuta anali ndi ena mwa akuluakulu achipani ku chigawo cha kummawa,pa boma komanso ku dera, kuphatikizapo m’modzi mwa amene alowa chipani cha MCP kuchokera ku DPP posachedwapa, a Imran Mtenje.

A Mtenje ati chipani cha MCP chili ndi zolinga zabwino zofuna kutukula dziko lino ndichifukwa chake sichikutekeseka ndi zomwe anthu otsutsa boma akukamba monyoza.

Iwo atinso kulowa kwa anthu ambiri m’chipanichi mchigawo  cha kummawa kukupereka umboni kuti mtsogoleri wadziko linoyu adzapambana mosavuta pa chisankho cha chaka chamawa.

M’modzi mwa amene alowa chipanichi ndi yemwe anali msungi chuma wachipani cha UDF, a Yusuf Shaibu, ndipo ati alowa chipani cha MCP chifukwa bomali likuchita zazikulu kumbali ya chitukuko.

 

Olemba: Mirriam Kaliza

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Police arrest reckless driver

Romeo Umali

Driemo roped in for Chitipa United dinner and dance

Yamikani Simutowe

BAM AGM aims to drive financial inclusion in rural areas

Arthur Chokhotho
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.