Malawi Broadcasting Corporation
Education Local Local News Nkhani

Ana opyola 1,000 asiyira sukulu panjira ku Lilongwe m’miyezi ya April mpaka June

Ana pafupifupi 1, 200 asiyira sukulu pa njira munzinda wa Lilongwe pakati pa miyezi ya April ndi June chaka chino chokha chifukwa cha umphawi komanso kuwachitira nkhanza, khonsolo ya mzindawu yatsimikiza.

M’modzi mwa akuluakulu a khonsoloyi, a Derrick Mwenda, ndi amene anena izi pa msonkhano okumbukira mwana wamu Africa kwa mfumu yayikulu Kabudula m’boma la Lilongwe.

Ndipo wa pampando wa khonsolo yomweyi, a Dominick Banda, anadzudzula m’chitidwe omwe sukulu zina zikuchita owumiriza ophunzira kupereka ndalama zapadera, zomwe ati zikukolezera kuti ana asiyire sukulu panjira.

A Chrissie Mbundungu omwe ndi m’modzi mwa adindo a bungwe la Organization for Sustainable Socio-Economic Development Initiative, ati bungwe lawo ndi lodzipereka kuonetsetsa kuti ufulu wa maphunziro ukufikira ana onse m’Malawi.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Tobacco sales at K677 billion

Trust Ofesi

MAFCO condemns players’ conduct

MBC Online

MBC HONOURS CHUNGA FOR INITIATING ENTERTAINERS OF THE YEAR PROGRAMME

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.