Bungwe lina lomwe ndi la atsogoleri a mipingo ya chisilamu ku Lilongwe lotchedwa Muslim Community lati ndilodzipereka kugwira ntchito ndi boma popititsa patsogolo chitukuko cha dziko lino.
Poyankhula ndi atolankhani ku Lilongwe mkulu wa bungweri Sheikh Mwalabu wati mipingo ndiyofunika kwambiri pa nkhani yachitukuko.
Sheikh Mwalabu ayamikira utsogoleri wa Prezidenti Chakwera poti waonetsera poyera kuti ndiofunira dziko lino zabwino ati poti ukugwira ntchito ndi mipingo yonse mdziko muno zomwe ati ndizofunika kwambiri pa chitukuko cha dziko.
Atsogoleriwa apemphanso nthumwi zomwe zikasankhe atsogoleri atsopano a chipani cholamula cha Malawi Congress kuti akasankhe mwanzeru makamaka atsogoleri omwe angathandizane ndi mtsogoleri wa dziko pa masomphenya ake.
Iye watinso kusapezeka kwa opikisana ndi a Chakwera pa msonkhanowu ndichitsimikizo kuti aliyense ndiokhutira ndi ulamuliro wake.