Mtsogoleri wa zokambirana za m’nyumba ya malamulo a Richard Chimwendo Banda ati nthawi yakwana ku chipani cha Democratic Progressive (DPP) kuti apatseko mpata achinyamata popereka maganizo pa zinthu zochitika mchipanichi komanso m’dziko muno.
A Chimwendo Banda ayankhula izi pamene amadzudzula a Joseph Mwanamvekha omwe ndi m’neneri wa zachuma ku chipani cha DPP kaamba konyazitsa dongosolo la chuma cha boma la chaka cha 2024/25.
A Mwanamvekha ati dongosololi silikupatsa chiyembekezo ati popeza ndalama zakunja zikupitilira kusowa, komanso kuti ngongole za boma zachuluka kwambiri.
Koma a Chimwendo Banda ati n’kosayenera kulankhula monyoza.
Olemba Margaret Mapando