Alimi a fodya a m’maboma a Kasungu ndi Dowa ati ndi okhutira ndi kuchuluka kwa kampani zogula fodya pa msika omwe watsegulira lero mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera.
Ena mwa alimiwa ati fodya wa kontalakiti komanso auction akumugula pa mitengo ya bwino kwambiri kusiyana ndi zaka zam’mbuyomo.
Iwo ati akugulitsa fodya wawo wa kontalakiti pansi pa kampani za Nyasa Tobacco, JTI ndi Alliance One, mwa ena.
Pomwe amatsekulira msika wa fodya wa chaka chino ku Chinkhoma m’boma la Kasungu, fodya amamugula pa mtengo wa $3.01 ndipo wotsika amafika pa $2.55.
Mabelo wokwana 2, 165 ndi omwe awagulitsa koma msikawu umatha kugulitsa mabelo 7,000 patsiku.
#MBCDigital
#Manthu