Boma lati achinyamata akuyenera kuphunzira mozama ntchito zaluso ndi cholinga chakuti masomphenya adziko lino a 2063 akhale aphindu.
Nduna yazachinyamata, a Uchizi Mkandawire, yalankhula izi ku Zomba pamwambo opereka ma Certificate kwa achinyamata pafupifupi 1000 amene atsiriza maphunziro osiyanasiyana antchito zaluso.
“Mundondomeko ya achinyamata, boma likutsindika kwambiri kukweza miyoyo ya achinyamata pachuma choncho zomwe zikuchitikazi ndi imodzi mwa ntchito zomwe unduna wathu ukulimbikitsa,” anatero a Mkandawire.
Mmau ake, mkulu wa bungwe la Care Malawi, Pamela Kuwali, wati ntchito ya Titukulane yapereka kusintha kwakukulu pakati pa achinyamata amaboma a Mangochi ndi Zomba kumbali yodzipezera chuma.
Bashir Ali, mmodzi wa achinyamata omwe apindula ndimaphunzirowa, wati umoyo wake wasintha pachuma kaamba ka ntchito yake yosoka, pansi pa ntchito ya Titukulane.
Olemba: Simeon Shumba


