Zadziwika kuti abambo okhala mdera la mfumu Mitundu ku Lilongwe akumadzipha kwambiri kaamba kosowa kumene angakatule nkhawa komanso kupeza upangiri pamavuto amene amakumana nawo.
Mmodzi mwa abambo okhala mderali, Francis Lupiya,alankhula izi pa msonkhano wa abambo umene unalipo Loweruka ndipo anakonza ndi a bungwe la Family Planning Association of Malawi pamodzi ndi bungwe la Men of Tomorrow ku Mitundu.
Mmodzi mwa akuluakulu a bungwe la, FPAM, a Vincent Sinda, anati abambo samalandira uphungu oyenera ngakhale ali mu khwimbi la anthu amene matenda a edzi komanso maganizo angwiro amawakhudza.
Mkulu wa bungwe la Men of Tomorrow, a Steven Mlangiza, analangiza abambo kuti apewe m’chitidwe odzipha powuzako anzawo zankhawa zimene akukumana nazo.