Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

A Sendeza alimbikitsa chilungamo pa ndondomeko ya Mtukula Pakhomo

Nduna yowona za chisamaliro cha anthu a Jean Sendeza yalangiza ogwira ntchito zolemba mayina anthu opindula ndi ndalama za Mtukula Pakhomo mdziko muno kuti aganizire anthu achikulire komanso awulumali akamachita kalembela wamayinawa.

A Sendeza anati anthu ochuluka akudandaula m’dziko muno kuti anthu ena oyenera kupindula ndi ndalamazi sakupindula.

Iwo anati sizoona kuwona anthu ochuluka pabanja limodzi loti litha kukwanitsa kupeza zofunikira pamoyo wawo kupindula nawo pamene mawanja ena ovutikitsitsa sakupatsidwa mwayi wamtunduwu.

Asendeza anena izi m’boma la Kasungu pamene iwo ndi komiti ya
kunyumba ya malamulo yolondoloza ntchito za chitukuko chaboma inayendela ena mwa mawanja omwe apindula ndi ndalama zamtukula pakhomo.

Wapampando wakomitiyi, a Noel Lipipa, wati ngakhale kuti ndondomeko ya mtukula pakhomo ikupindulira anthu ochuluka, ndondomekoyi ikukumanabe ndi mavuto ochuluka ndipo komitiyi ipitiriza kugwira ntchito ndi boma pothana ndi mavutowa.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Talandira K6 miliyoni koma siyokwanira — Silver Strikers

Emmanuel Chikonso

Lero tapereka holo-yi ndipo pompano tiyamba kumanga chipatala – Troughton

MBC Online

Masewero a lero ndi masamu — Kayira

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.