M’modzi mwa amene anali mamembala akuluakulu achipani cha DPP, a Ken Msonda, alowa chipani cha Malawi Congress (MCP).
A Msonda alandiridwa m’chipani cha MCP ku Mzuzu ndi mtsogoleri wachipanichi, Prezidenti Dr Lazarus Chakwera.
A Msonda anawapelekeza ndi mafumu akuluakulu aku Rumphi, kuphatikizapo mfumu yayikulu Chikulamayembe.
Poyankhula polandira a Msonda, Dr Chakwera adati khomo la chipani cha MCP ndi lotsekula ndipo onse amene akufuna kugwira ntchito ndi chipanichi ndi wolandiridwa.
M’mau awo, a Msonda anati MCP ndi chipani chokhacho chomwe chimatsata mfundo za dimokalase ndipo ndi okhutira ndi zitukuko zosiyanasiyana zimene zikuchitika m’dziko muno.
Ena mwa akuluakulu omwe adali nawo pamwambowo ndi a Harry Mkandawire, mkulu owona ndondomeko zachipani a Ken Zikhale Ng’oma, ndi m’modzi mwa magavanala a chipani cha MCP ku mpoto, a Kezzie Msukwa.