Malawi Broadcasting Corporation
Agriculture Local Local News Nkhani

Tisagulise chimanga chathu chidakali kumunda —Makwangwala

Mfumu yayikulu Makwangwala ya m’boma la Ntcheu yapempha anthu kuti asagulitse mbewu zawo, kuphatikizapo chimanga, isanakwane nthawi yokolola.

Mfumuyi yapempha izi potengera kuti alimi ena amakonda kugulitsa mbewu zawo kwa amalonda omwe amakhala akupereka ndalama ndi cholinga choti adzapatsidwe pa nthawi yokolola.

Malinga ndi Mfumuyi, mchitidwewu umasonkhezera njala pakati pa mabanja ambiri omwe amakhala kuti alibe chakudya, makamaka mmiyezi yakumapeto komanso kumayambiriro a chaka.

Iwo inawonjezeranso kupempha anthu kuti apewe mchitidwe womaphika zakudya mowononga pa nyengo ya zisangalalo zosiyanasiyana monga maukwati, zinamwali komanso kulonga maufumu.

Ndipo pothirirapo ndemanga pa nkhaniyi, anthu ena omwe anatenga nawo gawo mu programme ya the Pot pa MBC Radio One, anati akugwirizana kwathunthu ndi zomwe yapempha mfumuyi kaamba koti kawirikawiri anthu samalingalira za mabvuto a mtsogolo pomwe akugulitsa chimangachi.

 

Related posts

Drones in the Air at Chikangawa

Romeo Umali

Chimwendo warns against frustrating govt programmes

Rabson Kondowe

First Lady calls for collaboration in supporting needy students

Secret Segula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.