Malawi Broadcasting Corporation
Culture Local Local News Nkhani

Achewa athira nsembe

Anthu a chikhalidwe cha a Chewa athira nsembe ku Nsinja m’boma la Lilongwe ndipo apempha mphambe kuti akwaniritse zosowa zawo.

Kumwambowu, umene unalipo Loweruka, kunali anthu ochuluka amitundu yosiyanasiyana ya m’dziko muno komanso akuluakulu ochokera ku unduna wa zokopa alendo, unduna waza chikhalidwe ndi amene amayendetsa bungwe la Chewa Heritage Foundation, amene amatsogolera mwambowu.

Mwambowu ndi umodzi mwa miyambo ya a Chewa umene umachitika chaka ndi chaka ndipo umathandiza kubweretsa umodzi ndi mtendere pakati pa anthu amitundu yosiyana amene amakumana pa mwambowu.

Olemba: Ida Chiwaya

Related posts

K93BN programme to increase rural agriculture productivity

Rabson Kondowe

Assistant clerk of Parliament dies

Romeo Umali

MISA Malawi engages Mchinji Council on disinformation

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.