Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

‘Zitukuko zikufalikira ponseponse’

Mtsogoleri wa dziko wa lino, Dr Lazarus Chakwera, wati ndiokondwa kuti ntchito zachitukuko zikuyenda m’zigawo zonse komanso aMalawi akuyikapo chidwi, zimene zikusonyeza kuti dziko ndi la aliyense.

Iye adatsindika kuti chitukuko sichiyenera kukhazikika m’dera limodzi lokha.

Polankhula ku Zomba, mtsogoleri wa dziko linoyu wati mnzinda  wa Zomba uli ndi mbiri yopatsa chidwi, maka pa nkhani yazomangamanga zokhazikika, monga nyumba zomwe boma la Japan.

Pulezidenti Chakwera watsindikanso zakufunika kopereka mwayi wa ntchito kwa ophunzira amene adamaliza maphunziro awo kusukulu monga ya Domasi, ponena kuti sikwabwino kuti akhale pa ulova.

Ndipo Dr Chakwera alengeza kuti ayitanidwa ku Germany kumene, mwazina, akakambirana ndi mtsogoleri kumeneko zinthu zosiyanasiyana, kuphatikizapo za mayendedwe a sitima pa Nyanja ya Malawi.

 

Olemba: Mercy Zamawa

Related posts

Malawi ipindula ndi ntchito yotukula luso lazaumoyo

Romeo Umali

Voting starts for local government by-election in Mwasa Ward

Romeo Umali

Wanderers, Chitipa answer Airtel’s call with wins

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.