Nthumwi 1,100 zochekera mzigawo zonse za dziko lino za chipani cha People’s zikuyembekeza kusankha atsogoleri atsopano a chipanichi pa msonkhano waukulu wa chipanichi, umene uyambe masana ano munzinda wa Lilongwe.
Padakali pano, nthumwi zikulowa mchipinda momwe muchitikire msonkhano umenewu.
Wapampando wa komiti yomwe yakonza msokhanowu, a Peter Kamange, wati maina a omwe apikisane pa maudindo osiyanasiyana awatulutsa masana ano.
“Tikutsirizitsa ntchito younika maina a omwe apikisane. Anthu angapo apereka zikalata zoti apikisane pa udindo wa mtsogoleri wa People’s kotero tikatsiriza kuunika zipepala zomwe anthu apereka, titulutsa mndandanda wonse kuti anthu onse adziwe,” atero a Kamange.
Iwo ati zonse zili mchimake, ndipo akuyembekezera kuti msonkhanowu, umene uthe mawa loweruka, uyenda bwino.
Mutu wa msonkhanowu ndi ‘Restoring the Hope: Building a Brighter Future Together’.