Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Japan, WFP asainira mgwirizano othandiza dziko la Malawi pavuto la njala

Boma la Japan lithandiza dziko la Malawi ndi mpunga wa matani okwana pafupifupi 1900, amene ndi matumba oposa 30,000, kuti agawire anthu amene alibe chakudya m’dziko muno.

Poyankhula  munzinda wa Lilongwe, kazembe wadziko la Japan kuno ku Malawi, a Yoichi Oya, wati mpunga umene aperekewo,umene ndiwa ndalama zokwana K3.5 billion, ndichitsimikizo kuti Malawi ndi Japan ali pa ubale wabwino.

Mlembi ku nthambi yoona ngozi zogwa mwadzidzidzi, a Charles Kalemba, ayamika boma la Japan kaamba kathandizolo, lomwe lithandize maanja oposa 35,000 omwe alibe chakudya  kaamba kang’amba yomwe inali m’dziko muno.

Mkulu wa WFP kuno ku Malawi a Paul Turnbull ati aonetsetsa kuti pofika chaka cha mawa mu January, mpungawo ukhale utafika kuno ku Malawi

Boma linalengeza kuti maboma 23 ndi amene afunikire thandizo lachakudya ndipo anthu 5.7 million ndiwo alibe chakudya munyengo ino mpaka chaka cha mawa m’mwezi wa February.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Inhouse media signs Keli P

Romeo Umali

Mfumu yaikulu Nkhulambe yamwalira

Jeffrey Chinawa

ACTIONAID SET TO LAUNCH CLIMATE JUSTICE CAMPAIGN

McDonald Chiwayula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.