Nduna zosiyanasiyana zati zambiri mwa zomwe mtsogoleri wa dziko lino, Dr. Lazarus Chakwera, analonjeza kuti zichitike mu uthenga wawo wa SONA chaka chatha, zakwaniritsidwa.
Mwachitsanzo, nduna yowona za mtengatenga ndi ntchito zomangamanga a Jacob Hara yati misewu yambiri yomwe a Chakwera ananena mu SONA yapitayi yamangidwa.
A Hara anenanso kuti pakadali pano ntchito za njanji zomwe zinayiwalidwa m’mbuyomu zayambiranso ndipo mafuta ochuluka a galimoto abwera chaka chatha kudzera pa sitima zapanjanji.
Nduna yowona za madzi ndi ukhondo a Abida Mia nayo yati zitukuko zambiri zachitika.
Ndunayi yatchulapo ntchito monga ya Mangochi Nkhudzibay Water Project, yomwe yamangidwa ndikutsegulidwa pansi pa ulamuliro wa a Chakwera ndipo ikuthandiza mabanja oposa 92,000 m’boma la Mangochi.
Nduna ya zofalitsankhani a Moses Kunkuyu yati undunawu wapanga zitukuko zosiyanasiyana monga kukhazikitsa internet yaulere kudzera mu luso lamakono lotchedwa wifi mdziko muno.
A Kunkuyu ati lelo anthu ayembekezere kumva zitukuko zambiri zomwe boma litapange.
Wolemba Justin Mkweu