Dziko la Malawi latsegula ofesi ya ukazembe m’dziko la Israel kaamba kofuna kuti dziko lino lipindule ndi ntchito za ulimi ndi mtengatenga, mwa zina.
A Nancy Tembo omwe ndi nduna yoona za ubale wa dziko lino ndi maiko a kunja ati ofesiyi ndi yofunika chifukwa padakali pano achinyamata ambiri a m’dziko muno ali m’dziko la Israel ndipo ndikofunika kuti mdzikolo mukhale ofesiyi.
Malingana ndi a Tembo, ofesiyi ikhala mu mzinda wa Tel Aviv.
Nduna yoona za ntchito a Agness Nyalonje komanso nduna yofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu komanso nthumwi zina za dziko la Malawi ku Israel ndi ena ambiri, anali limodzi pamene ofesiyi amayitsegula.