Wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino, Dr Michael Usi, wachenjeza kuti boma sililekelera mchitidwe wachinyengo pakati pa akuluakulu amene akugwira ntchito yopereka chakudya ku mabanja omwe akubvutika ndi njala m’dziko muno.
Dr Usi alankhula izi mdera la mfumu yaikulu Chimwala m’boma la Mangochi pamene amatsogolera ntchito yopereka chimanga ku mabanja 1085 omwe akubvutika ndi njala mdera la Mkungulu m’bomalo.
Dr. Usi amayankhapo pa zomwe mkulu wa nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzi, DoDMA, a Charles Kalemba, anena kuti mmadera ena monga Blantyre ntchito yogawa chakudya yakumana ndi mabvuto osiyanasiyana monga chinyengo panthawi yolemba anthu omwe akuyenera kulandira thandizo.
Dr Usi ati boma lionetsetsa kuti aliyense opezeka akusokoneza ndondomeko yaboma yogawa chakudya, lamulo ligwira ntchito.
Paulendowu, Dr Usi akugawanso chakudya kumabanja obvutika m’dera la mfumu yaikulu Msamala m’boma la Balaka.
Ntchitoyi ikuchitika pansi pa ndondomeko ya nthambi ya DoDMA yopereka chakudya ku mabanja obvutika kuyambira mwezi wa December mpaka March chaka cha mawa.
Olemba: Owen Mavula