Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Yemwe akumuganizira kuti anapha mlonda wa Ichocho, amugwira

Apolisi ku Soche mumzinda wa Blantyre amanga Simple Jeputala wazaka 28 pomuganizira kuti anapha mlonda,  Leyona Yona kenako ndikuba pamalo pomwe mlondayo amagwira ntchito.

Mneneri wapolisi ku Soche Aaron Chilala wati malemu Yona amagwira ntchito ku kampani yachitetezo ya Ichocho ndipo Jeputala nayenso anagwirapo ntchito ku kampani yachitetezo ya Ichocho koma anasiya ntchitoyo.

Patsikulo, malemu Yona amalondera pa malo osungira katundu a Anena Anena Logistics ndipo Jeputala analonderaponso pamalopo panthawi yomwe amagwira ntchito kwa Ichocho.

Kenako gulu la mbava, kuphatikizapo Jeputala linafika pamalopo usiku ndikumenya mlondayo. Munthu wina yemwe anapita pamalopo kukasiya katundu mmawa, ndiye anapeza thupi la mlondayo.

Pakadali pano, apolisi akufufuza komwe kuli amzake a Jeputala.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

‘Tidzibweretsa malita 2 million pa ulendo umodzi’

Beatrice Mwape

Burning Spear wapereka mphatso ya gitala kwa President Chakwera

MBC Online

Banja lapha mwana pofuna kulemera

Charles Pensulo
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.