Unduna wazofalitsa nkhani wati ndiokhutira ndi m’mene MB ikugwirira ntchito zake pokwaniritsa zokhumba za aMalawi onse m’dziko muno.
Mlembi wamkulu mu undunawu, a Baldwin Chiyamwaka, ati ndizosangalatsa kuti madandaulo amene anthu mmbuyomu anali nawo pa mapologalamu a MBC tsopano anachepa kwambiri, kutanthauza kuti bungweli likuyesetsa.
A Chiyamwaka anena izi atayendera maofesi a MBC ku Blantyre ndikuona zipangizo zomwe MBC ikugwiritsa ntchito powulutsa mawu.
Iwo ati undunawu upitiriza kuthandiza MBC munjira zosiyanasiyana kuti ikwaniritse zolinga zake zofikira aMalawi onse.