Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

World Bank yaonetsa chikhulupiliro ku boma la Malawi

Nduna yoona za maboma ang’ono, umodzi ndi chikhalidwe cha anthu a Richard Chimwendo Banda ati thandizo la ndalama zokwana $80 million ndi chitsimikizo choti World Bank ndi yokhutira ndi momwe boma likuyendetsera dzikoli ngakhale panali mavuto osiyanasiyana pakatipa.

Polankhula pa bwalo la Dowa Community, a Chimwendo Banda ati boma laonetsa kudzipereka pa ntchito za ulimi wa minda ikulu ikulu, kumangila asilikali nyumba, kupereka 200 million zachitukuko kudera la phungu aliyense, kulambula ndikupaka phula misewu mwa ntchito zambiri ngakhale dzikoli linakumana ndi ngozi zosiyanasiyana.

Iwo atinso alimi a fodya akuyimba lokoma kwa nthawi yoyamba patapita zaka zambiri kaamba koti akugulitsa fodya wawo pa mtengo wabwino.

Iwo analangizanso atsogoleri andale kuti apewe ndale zonyozana, ati kaamba koti zimadzetsa zipolowe.

Wapampando wa chipani cha Malawi Congress mchigawo cha pakati, a Patrick Zebron Chilondola, ati zonse zokonzekera msonkhano waukulu wa chipanichi mu August muno zikuyenda bwino.

Wolemba: Isaac Jali

Related posts

Boma lasintha alembi ena muma unduna

Alinafe Mlamba

Anthu ochuluka asonkhana ku maliro a Hope Chisanu

Romeo Umali

Chotsani katangale pa ndondomeko yothandiza anthu — DoDMA

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.