Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress (MCP), a Catherine Gotani Hara, wayamikira mtsogoleri wa chipanichi komanso dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, ponena kuti ndiodekha komanso ochita zinthu mwa dongosolo.
Iwo amayankhula izi m’boma la Rumphi pa bwalo la masewero a Polisi ya Rumphi pamene amawatsimikizira anthu okonda chipani cha MCP kuti boma la Dr Chakwera ndi lokonzeka kumalizitsa ntchito zachitukuko zosiyanasiyana m’dziko muno.
A Gotani Hara anakambapo pa nkhani za misewu kuti ntchitozi zikuoneka ngati zikuchedwa malo ena kaamba kakuti boma likufuna kumanga zinthu zolimba zomwe ndi zokomera aMalawi onse pothandiza ntchito zambiri zachitukuko kuphatikizapo malonda.
Olemba: Jackson Sichali