Phungu wadera la kumadzulo m’boma la Mwanza, Joyce Chitsulo, wayamikira boma chifukwa chogawa chitukuko mosayang’ana chipani.
A Chitsulo, amene ndi phungu wa chipani cha Democratic Progressive (DPP), anena izi pa sukulu ya sekondale yoyendera ya Thawale kwa Mfumu yaikulu Nthache ku Mwanza pa mwambo wokhazikitsa ntchito yomanga malo a luso lamakono la ICT.
Iwo ati monga phungu wambali yotsutsa, boma likanatha kuyamba madera ena komwe kuli aphungu ake. Iwo anena izi popeza ndime yoyamba yantchito yomanga malo amakonowo ndi ya sukulu zokwana 75 zokha.
Nduna yofalitsa nkhani, a Moses Kunkuyu, yati luso lamakono ndi imodzi mwa msanamira za chitukuko za Malawi 2063, choncho nkofunika kufikira madera onse ndi ndondomekoyi.
Bungwe la Malawi communications Regulatory Authority lomwe likugwira ntchitoyi kudzera mundondomeko yotchedwa connect a school, lalonjeza kuti ntchitoyo ayigwira kwa miyezi itatu.