Nduna yoona za ulimi a Sam Kawale yauza alangizi kuti adzitenga gawo lalikulu losintha kaganizidwe ka anthu ndi cholinga chothana ndi vuto lakusowa kwa chakudya m’dziko muno.
A Kawale ayankhula izi pamkumano wapakati pa akuluakulu a boma ndi alangizi ochokera m’chigawo cha kummwera kumene kuli alangizi opyola 500 komanso akuluakulu a bungwe la NEEF.
Iwo anati imodzi mwanjira yodalirika yomwe ingathane ndi vuto lakusowa kwa chakudya ndi kuyambapo kuphunzitsa anthu ulimi wamakono olima mbewu zochuluka ndi kumadzazigulitsa kumisika ya m’dziko muno komanso ya mayiko akunja.
Ndunayi inapitiriza kufotokoza kuti ichi ndi chifukwa chake boma tsopano lachilimika kwambiri kuti alimi ochuluka akhale ndi mwayi otenga ngongole kuchokera ku bungwe la NEEF mmalo mongodalira feteleza otsika mtengo.
Izi anati zidzathandiza kwambiri kuti dziko lino lidzakhale ndi chakudya komanso mbewu zochuluka zimene zidzathandizenso kwambiri pachuma cha dziko, makamaka pomapeza ndalama zambiri za m’maiko akunja.