Galimoto yomwe yanyamula malemu Dr Saulos Chilima kubwalo lazamasewero la Bingu National lanyamuka pa mdipiti kupita kumudzi kwawo kwa Mbirimtengerenji mdera la mfumu yaikulu Champiti ku Nsipe m’boma la Ntcheu.
Prezidenti wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera komanso mayi wa dziko lino Madam Monica Chakwera ndiwo anatsogolera mtundu wa a Malawi popereka ulemu wotsiriza kwa malemu Dr Chilima.
Thupi la Malemu Dr Chilima akaliyika m’manda mawa Lolemba, lomwe a Prezidenti a dziko lino akhazikitsa kuti likhale tsiku la tchuthi.