Alimi a m’mudzi wa Simone mdera la mfumu yayikulu Nankumba m’boma la Mangochi apempha boma kuti liwathandize ndi zipangizo zolimbikitsa ulimi wa mnthilira.
Alimiwa, amene amalima pa gulu limene amalitcha kuti Ndokela, apereka pempholi kudzera kwa wachiwiri kwa nduna ya zaulimi, a Benedicto Chambo, amene anali pa ulendo oyendera minda ikuluikulu yomwe akuyendetsa ndi anthu okhala m’bomali.
Paulendowo, zadziwika kuti alimi ochuluka ali ndi chidwi cholima minda ikuluikulu koma chimene akufuna ndi chilimbikitso komanso upangiri okwanira.
Mmodzi mwa iwo, a Samson Lester, anati “talima chimanga chokwanira mahekitala 20 kudalira ulimi wamvula, koma boma litatithandiza ndi makina opopera madzi titha kulima chimanga komanso mpunga ochuluka kudzera ku ulimi wa nthilira”.
Mmawu awo, a Chambo anati mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera ndi yemwe adakhazikitsa ndondomeko zaulimi wa minda ikuluikulu kuti dziko lino lisamavutike ndi njala.
A Chambo anatsindikanso kunena kuti unduna wawo uwonetsetsa kuti alimiwa komanso alimi onse m’dziko muno akuthandizidwa munjira zosiyanasiyana.