Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Timu ya Draughts yalephera kupita ku Russia

Timu ya masewero a Draughts ya dziko lino yalephera kupita kukasewera nawo mpikisano wa dziko lonse kaamba kochedwa kukonzekera.

Mlembi wa bungwe loyendetsa masewero wa m’dziko muno la ADIMA, Suzgo Nkhoma, wauza MBC kuti anachedwa kuchititsa mpikisano opeza akatswiri opita ku Russia kaamba kosowa ndalama ndipo izi zachititsa kuti alephere kupangitsa ma VISA a osewerawa mu nthawi  yabwino.

Osewera okwana asanu ndi amene amayenera kupita ku mpikisanowo.

A Nkhoma ati padakali pano, chidwi chonse ayika pa mpikisano wa m’mayiko a mu Africa omwe uchitike mwezi wa November m’dziko la Zimbabwe.

 

Olemba Amin Mussa

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

President Chakwera in Kenya for Fertilizer and Soil Health Conference

MBC Online

Japan to help Malawi eliminate poverty

Rabson Kondowe

Self Help Africa winds up mission in Dedza

Sothini Ndazi
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.