Mmodzi wa anthu ochita malonda ogulitsa zakudya zophika zachi Malawi a Aubrey Daza, amene ndi mwini wa malo odyera a Chanza Take Away m’boma la Ntcheu, wati nawo amalonda ang’ono ang’ono mgawo lawoli akuthandiza pantchito zokopa alendo.
Iwo anena izi pomwe mwezi uno, dziko lino likukumbukira ntchito zokopa alendo.
A Daza ati pakadali pano, a Malawi ambiri anamvetsesa ubwino wa kudya zakudya zachikhalidwe, zimenenso zikuchititsa kuti ntchito zawo ngati amalonda zidziyenda bwino.
Mmodzi mwa anthu amene tinakumana nawo pa malowa, a Julius Phiri, amene anali pa ulendo ochokera mu mzinda wa Mzuzu, anati ndiokhutira ndi momwe malo ang’ono ang’ono ngati otere akulimbikitsira ntchito zokopa alendo pogulitsa zakudya zachiMalawi.
Wolemba: Geoffrey Chinawa ndi Chisomo Break