Malemu Mfumu Yaikulu Amidu awayika mmanda lero ku likulu kwa ufumu wawo ku Nangulungutiche ku Balaka.
Mfumuyi dzina lawo lenileni linali Amina Gayesi ndipo anamwalira ali ndi zaka 56 Loweruka lapitali pa chipatala chachikulu cha Zomba atadwala nthenda ya khansa.
Pamwambowo, mlembi wamkulu ku unduna wazamaboma ang’ono, Elizabeth Chindebvu, anati unduna wawo ndiokhudzidwa ndi imfayi chifukwa mtsogoleri akachoka pamalo,chitukuko chimasokonekera.
Iwo anapempha banja lofedwa kuti lisunge bata ndi mtendere mpaka atasankha mlowammalo amene aliyense adzakhutire naye.
Wachiwiri kwa wapampando wa khonsolo ya Balaka, a Dickson Wasili, anati iwo ndiodandaula potaya mfumu yokhayo yachizimayi imene inatsala m’bomalo.
Malemu T/A Amidu asiya ana anayi.
Olemba: Mirriam Kaliza