Apolisi ku Limbe mu mzinda wa Blantyre amanga anthu anayi powaganizira kuti anathyola sitolo ndikuba zipangizo za galimoto, kuphatikizapo mabatire.
Wachiwiri kwa ofalitsankhani zapolisi ku Limbe, Chibisa Mlimbika, wati anayiwo anafika pamalo pomwe pali ofesi za kampani ya zomangamanga ya Dika Construction House ndipo anamanga mlonda asanathyole ndikuba zipangizozo.
Anthu anayiwo ndi Saidi Mambo wazaka 32, Victor Chamasowa wazaka 28, Patrick Chingwalu wazaka 25 ndi Andrew Juma wazaka 26.
Kafukufuku wa apolisi waonetsa kuti mbavazo ndi zomwenso zinakaba
zipangizo za galimoto zandalama pafupifupi K2 million kunyumba ina ku Kanjedza mumzinda womwewo wa Blantyre.