Pamene chipani cha UTM chikukonzekera kudzachita msonkhano wake waukulu mwezi wa mawa, mlembi wamkulu wa chipanichi, a Patricia Kaliati, alengeza kuti adzapikisana nawo pa udindo wa mtsogoleri.
Kudzera pa tsamba lawo la mchezo la Facebook, iwo ati ali ndi ukadaulo pa nkhani za ndale potengera kuti akhala akugwira ntchito m’boma mmaudindo osiyanasiyana kuyambira m’chaka cha 1994 ndipo ali ndi chikhulupiliro kuti atha kukwanitsa kutsogolera chipanichi mosavuta.
Msonkhano waukuluwu udzachitika pa 17 November chaka chino.
Wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino, Dr Michael Usi, ndiye mtsogoleri wa chipani cha UTM.
Olemba: Alufisha Fischer