Nduna ya zaumoyo, a Khumbize Kandodo Chiponda, yapempha anthu m’dziko muno kuti apewe m’chitidwe wa katangale ndi ziphuphu pofuna kupeza ndi kupereka thandizo la zaumoyo m’zipatala zosiyanasiyana.
Iwo ayankhula izi pamwambo otsekulira chipatala cha ching’ono cha Milamba chimene bungwe la Press Trust lamanga ku Nkhoma m’boma la Lilongwe ndi ndalama zokwana K165 million ndipo anthu oposa 30, 000 m’derali ndi amene akuyenereka kupindula.
Ndunayi inati masomphenya a dziko lino a Malawi 2063 ndi otheka ndipo anapempha anthu m’dziko muno kuti agwirane manja pofuna kutukula ntchito zaumoyo.
M’modzi mwa akuluakulu ku bungwe la Press Trust, a Wilson Chirwa, anati masomphenya awo ndi kutukula ntchito zaumoyo m’dziko muno.
Phungu wa Lilongwe Mpenu, a Collins Kajawa, anati awonetsetsa kuti anthu a m’derali akusamala chipatalachi.
Olemba: Thokozani Jumpha