Akuluakulu a malo ogona alendo a Mount Soche munzinda wa Blantyre ati akwanitsa kuzimitsa moto umene unabuka pamalowo.
Malinga ndi mmodzi mwa akuluakuluwo, motowo unabuka ku malo komwe amatayako zinyalala.
Iwo ati motowo sunakhudze malo eni-eni ogona alendo.
Pakadali pano, akuluakuluwo apempha alendo komanso ogwira ntchito amene anathawa pamalopo kuti abwelere, ponena kuti palibe chiwopsezo chilichonse.