Alimi a ng’ombe za mkaka m’chigawo cha ku m’mwera apempha madalaivala agalimoto zikuluzikulu kuti asiye kunyanyala ntchito chifukwa akutaya mkaka wambiri.
Dzulo lokha, alimiwa ati ataya malita 240 sauzande omwe ndi wa ndalama zokwana pafupifupi K120 million kaamba kakuti galimoto zikuluzikulu zonyamula mkaka sizikuyenda.
Poyankhula pa msonkhano wa olembankhani kwa Bvumbwe m’boma la Thyolo, wapampando wa Farmers Milk Producers Association (FAMPA), a Foster Mulumbe, anati akufuna zokambirana zipitilire pakati pa magulu onse okhudzidwa pa nkhani yonyanyala ntchitoyi uku ntchito zina zonse zikuyenda.
A Mulumbe anati izi zili chomwechi chifukwa alimi awo akusowa mtengo ogwira.
Lachitatu, madalaivalawa amanyanyala ntchito yawo pofuna mabwana awo kuti awakwezere malipilo awo apa mwezi, mwa zina.
Olemba: Geoffrey Chinawa