Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Mafumu asayina mgwirizano wa chitukuko ndi kampani ya Globe Metals and Mining

Mafumu a m’maboma a Mzimba ndi Kasungu asayinira mgwirizano ndi akuluakulu a kampani ya Globe Metals and Mining womwe uthandize kuti anthu a mmadera ozungulira mgodiwu apindule pa chitukuko cha mgodi wa Kanyika, omwe uli m’dera la Inkosi Mabilawo m’boma la Mzimba.

Mlendo wolemekezeka pa mwambowu, Inkosi ya Makhosi Mmbelwa yachisanu, inayamikira magulu awiriwa posayinira mgwirizanowu ndipo inapempha anthu mderali kuti agwirizane kuti derali lipindule ndi ntchitoyi.

Boma la Malawi linasayinira kale mgwirizano ndi Kampani ya Globe Metals and Mining chaka chatha.

Kusayinira kwa mgwirizanowu pakati pa mafumu ndi kampaniyi ndi imodzi mwa ndondomeko zomwe zili mmalamulo atsopano a zamigodi, Mines and Minerals Act 2023.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Chilemba waona nyenyezi ku Russia

Emmanuel Chikonso

‘Nsomba zipezeke komanso zotsika mtengo’

Beatrice Mwape

President Chakwera wati atsogoleri a mipingo ali ndi ntchito yayikulu

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.