Chikho cha mpira wa miyendo cha Tambala Super tsopano achikhazikitsa ndipo adzipikisana ndi matimu ang’onoang’ono a m’boma la Blantyre.
Chikhochi ndi cha ndalama zokwana K10 million zomwe inayikapo ndi kampani ya Amazone Group Limited.
Mkulu wa kampaniyi, a Moses Kunkuyu, anati anaganiza zothandiza chikhochi m’boma lonse la Blantyre popeza iwo ndi nzika yomwe ili ndi mbiri m’madera onse a m’bomali.
Masewero okhazikitsa chikhochi anali apakati pa timu ya Chikuli Young Eagles yomwe inagonjetsa Kumanda All Stars 10-9 pa mapenote atalepherana kugoletsana m’zigawo ziwiri za masewerowa.
Gulu la Black Missionaries komanso Simon ndi Kendal anasangalatsa anthu ndi mayimbidwe pamwambowo.