Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Othamanga akufuna kuthandiza ntchito za umoyo kudzera m’masewero

Gulu la othamanga lotchedwa ‘Joggers on the move’ latolera ndalama zokwana K10 million zomwe akufuna kuti agwiritse ntchito poika magetsi a mphamvu ya dzuwa pa chipatala cha Matekenya m’boma la Dowa.

Wapampando wa bungweli, a Chisomo Kalumura, ati iwo akufuna ndalama zokwana K13 million ndipo ati ali ndi chikhupiliro kuti akwanitsa kuyitolera.

Iwo ati izi zili chomwechi kaamba koti ndalama zina azitolera pa mpikisano othamanga umene omwe ukathere munzinda wa Lilongwe pa Gateway Mall loweluka likudzali.

A Kalumura anayankhula izi atalandira thandizo la ndalama zokwana K2 million kuchokera ku kampani ya Lab20 ku ntchito yofuna kuika solar pa chipatala cha Matekenya.

Mkulu wa zamalonda ku kampaniyi, a Brian Banda, ati apereka thandizoli kaamba koti bungwe la anthu othamangawa likuchita zofunikira ndipo anati zithandiza kupulumutsa miyoyo ya anthu ambiri ku Dowa.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

FAM ikusaka ma passport a Flames

MBC Online

Boma likuyika maziko a chitukuko — Dr Chakwera

MBC Online

Anthu okhudzidwa ndi madzi osefukira ku Nkhotakota akufuna thandizo lochuluka

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.