Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

Usi atsekulira msonkhano okambirana za magetsi

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Michael Usi, atsekulira msonkhano waukulu wa chaka chino okambirana njira zolimbikitsa anthu kugwiritsa ntchito magetsi oyendera mphamvu ya dzuwa ndi zinthu zina munzinda wa Lilongwe.

Msonkhanowu ukuchitika pamene dziko la Malawi likupanga 500 megawatts yomwe yathana ndi vuto lakuzima kwa magetsi.

Komabe, akatswiri akuti n’kofunika kuti magetsi afikirebe m’madera ambiri akumidzi kaamba koti magetsi ndi gwero la chitukuko.

Zaka zingapo zapitazo, makina opanga magetsi adawonongeka ndi namondwe ku Tedzani, zomwe zachititsa kuti boma pamodzi ndi mabungwe alimbikitse njira zina monga magetsi a dzuwa ndi mphepo m’malo mongodalira magetsi a mphamvu ya madzi.

Olemba: Isaac Jali

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

GOVT PLEDGES TO SUPPORT CREATIVE INDUSTRY

MBC Online

Living Waters Church feeds senior citizens

MBC Online

MALAWI TO RAISE K15 BN FROM CEMENT

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.