Mkulu wa ntchito za ndende m’chigawo cha pakati, a Bazirial Chapuwala, walamula ogwira ntchito ku ndende za m’chigawochi kuti adzipereka thumba la chimanga la 50 killogramme kwa amene azigwira mkayidi amene wathawa ku ndende.
“Mukawona mkayidi kapena akayidi asanu akathawa, muziwona thumba la chimanga. Amene wakwanitsa kugwira mkayidi, adzipita kwa akuluakulu a ndende ku kalandira thumba la chimanga,” a iwo anatero.
A Chapuwala, amenenso ndi wachiwiri kwa komishonala oyang’anira ndende m’dziko muno, ayankhula izi pa mwambo okondwerera chaka cha tsopano wa ogwira ntchito ku nthambiyi m’chigawo cha pakati ku Nalikule Teacher’s College munzinda wa Lilongwe.
Iwo anatsindika kuti dipo la thumba la chimanga adzipereka kwa anthu wamba, osati ogwira ntchito ku nthambi za chitetezo, monga Police ndi Malawi Defence Force.
A Chapuwala ati akufuna pakhale ubale wabwino pakati pa ogwira ntchito ku nthambiyi ndi anthu okhala mozungulira ndende ndi madera ena, kuti chitetezo chikhale chokhwima.
Kotero iwo achenjeza kuti nthambiyi ithana ndi ma ofesala amene apezeke akuchita za chinyengo komanso osasunga mwambo.