Mtsogoleri wa Mpingo wa Salvation for All Ministries International, m’busa Clifford Kawinga, wapempha mabungwe ndi amipingo kuti agwirane manja pothandiza anthu omwe akhudzidwa ndi njala m’dziko muno.
A Kawinga anena izi pamene amagawa matumba achimanga kwa anthu 1,200 komanso kulalikira uthenga wa Mulungu m’dera la mfumu yaikulu Matola m’boma la Balaka.
M’busayu wati apitiliza kutumikira anthu powalalikira komanso kuthandiza zosowa zawo za thupi.
Iwo anagawanso ma Baibulo kwa mafumu ndi atsogoleri osiyanasiyana.
Wolemba: Blessings Cheleuka