Ntchito yomanga ofesi ya tsopano ya khonsolo ya Mangochi akuti ithandiza kwambiri m’mene adindo amagwilira ntchito.
Izi zili chomwechi kaamba koti adindo anthambi zambiri zofunikira adzigwira ntchito pamalo amodzi kusiyana ndi mmene zinthu zilili pano pamene ofesi zili mbali ina ya town ya Mangochi.
Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, masanawa anayendera ntchito yomanga ofesiyi ndipo anabzyalapo mtengo.
Pakadali pano, Dr Chakwera ndi Mayi Monica Chakwera anyamuka ulendo opita kukayendera ntchito yomanga msewu wa Monkey Bay – Cape Maclear.
Olemba: Owen Mavula