Mlangizi wa prezidenti pa ndale a Kingsley Sulamoyo ati mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera wataya kholo mu uzimu pa imfa ya the Very Reverend Killion Mgawi.
A Sulamoyo, omwe ayankhula mmalo mwa Dr Chakwera, ati panthawi yomwe mtsogoleri wa dziko linoyu anali pa sukulu ya ubusa, anakhala limodzi ndi abusa a Mgawi ndipo amawalangiza ndi kuwaunikira m’magawo osiyanasiyanasiyana.
A Sulamoyo ati Dr Chakwera ndiothokoza kuti abusa a Mgawi asiya anthu odalirika omwe akugwira ntchito zikuluzukulu mothandizana ndi a Prezidenti kuyendetsa dziko lino.
Iwo apempha a Malawi kuti aphunzire pa momwe abusa a Mgawi akhalira moyo wawo pa dziko pano.
Mtsogoleri wa dziko lino wapepesa banja la a Mgawi pa imfayi ndi ndalama yokwana K2 million.