Mmodzi mwa anthu odziwika bwino pandale, a Vitumbiko Mumba, wati nthawi yakwana yoti achinyamata azindikire kufunika kolembetsa mkaundula wavoti ndikutenga nawo gawo pankhani zandale m’dziko muno.
A Mumba ayankhula izi pokonzekera mwambo wa mayimbidwe wa ulele omwe akonza loweruka lino pa bwalo lazamasewero la Civo munzinda wa Lilongwe.
Mwambowu aukonza pamutu oti ‘Chakwera Kutchaya Kugwetsa Youth Concert’.
Iwo atinso iyi ndi mbali imodzi yomema achinyamata kukalembetsa ndikuwadziwitsa zakufunika kolembetsa kaamba koti chiphaso cholowera kuphwandoli ndi kalata yosonyeza kuti walembetsa mkaundula wavoti.
Oyimba monga Jetu, Kelly Devine Njuchi, Don Tarz, Merchah, Prince Chitz, Emmie Deebo, Symon and Kendal, Lulu, Skeffa, Dan Lu, Malinga, Chizmo Njuchi, Afana Ceez, Blasto ndi Born Afrikan adzakhala nawo.