Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Ntchito yopanga ziphaso ku Mangochi ikutheka

Anthu okhala m’boma la Mangochi ndi maboma ena ku chigawo cha kumvuma tsopano ali ndi kuthekera kopangitsa zitupa zoyendera nthambi ya Immigration italengeza kuti iyambiranso kugwira ntchito yopereka ziphaso ku ofesi zake m’boma la Mangochi kuyambira pa 20 August, chaka chino.

Ofalitsa nkhani ku nthambiyi, a Wellington Chiponde, anati kuyambiranso kwa ntchitoyi kuthandiza anthu okhala m’madera akumvuma kwa dziko lino kuti adzilembetsa komanso kulandira ziphasozi mosavuta.

Izi zikutanthauza kuti tsopano ofesi zonse za nthambiyi zayamba kugwira ntchito.

“Ife takhala tikunena kuti tikuchita chothekera kuti ntchito yopereka zitupa m’dziko muno izigwirika mwachangu ndipo momwe zateremu ndiye kuti zonse zili bwino,” a Chiponde anatero.

Mangochi ndi limodzi mwa ma boma omwe nzika zake zimakonda kupita maiko akunja monga ku South Africa kukachita malonda komanso kugwira ntchito.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

A Ken Msonda alowa chipani cha MCP

Chisomo Manda

Titukule sukulu za mkombaphala – Joe Ching’ani

MBC Online

Illovo itolera ndalama zolimbikitsa ukhondo wa atsikana msukulu

Lonjezo Msodoka
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.