Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Michael Usi atsimikizira anthu aku Mulanje kuti alandira ngongole zoti achitire bizinesi ndicholinga chotukula miyoyo yawo.
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko linoyu wapemphanso anthu kuti alimbikitse umodzi pa chitukuko.
Iwo ati adindo akuyenera alembe anthu ochita bizinesi zing’onozing’ono mosayang’ana chipani kuti aliyense apindule.
Pa nkhani ya chakudya, Dr Usi ati iwo ali okonzeka kuthandiza anthu achikulire mdera lakwa Golden ndi chakudya pomwenso bungwe la DODMA likhale likuthandiza anthu ndi chakudya, maka omwe alibiletu.