Zidutswa za ndege imene inasowa itangonyamuka kumene pa bwalo la ndege la Vachkazhets m’dziko la Russia azipeza.
Malinga ndi unduna owona za ngozi zogwa mwadzidzidzi m’dzikolo, anthu 17 afa pa ngoziyi ndipo ena asanu sanawapeze.
Ndegeyi inanyamula anthu 22.
Padakali pano, ntchito yoyang’ana anthu amene sanawapeze idakali mkati.
Olemba: Alufisha Fischer