Chiwerengero cha anthu amene akukhudzidwa ndi bvuto losowa chakudya kaamba ka mavuto odza chifukwa cha kusintha kwa nyengo m’chigawo cha SADC chafika pa anthu 67.7 million kuchokera pa 57.1 million m’chaka cha 2023.
Izi ndi malinga ndi lipoti la akatswiri oona za nyengo m’chigawochi limene alitulutsa posachedwapa.
Akatswiriwa amayankhula izi pa msonkhano wawo womwe unachitika kuyambira pa 26 mpaka pa 28 August chaka chino.
Iwo amakumana pa chaka kawiri kuti agawane zomwe apeza pa zanyengo maka m’chigawo cha maiko akumwera muno mu Africa.
Olemba: Alufeyo Liyaya