Bungwe la Malawi Union of Savings and Credit Cooperatives (MUSCCO) lati chuma chama SACCO tsopano chakwana K82 billion chaka chino chokha kuchokera kwa mamembala okwana 239,000 m’dziko lino.
Kutsatira izi, m’modzi mwa akuluakulu a bungweli, a Daniel Infa, amema aMalawi kuti adzisungitsa ndalama ku nthambi zawo pofuna kuchulukitsa makobili.
Izi zidadziwika loweruka pa msonkhano wa pa chaka wa nthambi ya Kasupe SACCO mu mzinda wa Lilongwe.
Mtsogoleri wawo, a Philip Kaingo, anatsimikiza kuti iwo akuchita phindu chifukwa akwanitsa kuchulutsa ndalama zawo, kuphatikizirapo katundu, zomwe ndi zokwana K254 million kuchoka pa K209 million.
A Kaingo anaonjezerapo kunena kuti padakali pano akwanitsa kutorera ndalama zokwana K18 million pa mamembala okwana 431.