Mmodzi mwa akuluakulu a chipani cha Malawi Congress Party (MCP) m’chigawo chakum’mwera, a Brown Mpinganjira, apempha anthu a m’boma la Thyolo kuti asamaope kapena kuopsezedwa ndi anthu a zipani zina akafuna kulowa chipani cha MCP.
A Mpinganjira amayankhula izi kwa Bvumbwe m’bomali pamene amapereka zovala za makaka a chipani cha MCP monga ma T-Shirt ndi nsalu.
Iwo anapitirizanso kunena kuti dziko la Malawi ndi lazipani zambiri ndipo anthu ali ndi ufulu olowa chipani chomwe angafune.
A Mpinganjira apemphanso anthu kuti adzavotere aphungu a MCP mu chisankho cha mchaka cha 2025.
By Alufisha Fischer.